#Mzimu ya zochitika,chonde bisani dzina langa,ine ndikufuna ndinve - TopicsExpress



          

#Mzimu ya zochitika,chonde bisani dzina langa,ine ndikufuna ndinve maganizo a fans pa page lako ili. Ayise zochitika,nkazi wanga amakonda kwambili kumaonesa mabere [Displaying breast] Ndakhala ndikumuudzapo zamuchitidwe wake kuti asiye koma iye amati ndi pomwe zovala zake amapangira Matsiku ano,ngakhale Mlongo wanga amandikalipiratso kuti zomwe ndikudandaula ndi zosaveka,anzanga nawo ambili amati palibe nchifukwa nkazi kumaonetsa mbali dzina zabele,iwo akuti izi zili mu fashion ndipo ndi ankazi ambili akupanga chonchi.#Zochitika ine zimandikhumudwitsa kwambili,kodi ndi bwino kuti nkazi wanga azitero?sindikufuna kumaonetsa ngati wovuta kapena wa nsanje. Ili ndi funso lomwe wafunsa Zanthu waku Malawi,ndipo tatenga ma photo ena monga chisadzo chokhudzana ndi momwe wafusira.Tiyeni nawo mayankho. No fear No favour. Zochitika pa Capetown
Posted on: Thu, 02 Oct 2014 15:08:08 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015