ANAMFEDWA AMENYANA KU CHIRIMBA - BT Ampingo anali atalalika - TopicsExpress



          

ANAMFEDWA AMENYANA KU CHIRIMBA - BT Ampingo anali atalalika ndikumaliza. Nawo amfumu, anamfedwa analankhula za bambo Makuluni amene anali atatsogola. Kenako mwambo wokwilira bokosi unayambika, basi anthu adangowona first born wa malemu Makuluni wadumphira mu dzenje mo ali ndifuna mundikwilira limodzi ndi madala anga. Akuluakulu kubwera kumunyengelera mnyamata sadzatheka. Basi uyu ali mu dzenje momo, ntchito yokwilira itayima, ngono wake adabwera chapompo ndikumuwuza kuti achoke mudzenjemo kuti adzukulu apitilize ntchito. Kodi chamba chija umasutira kuti uzavute kuno? anafunsa mokwiya wangonoyu Ndiyetu basi man amakana kutuluka mu dzenje wa anatulukamo mokwiya ndikumushava mbama mbale wakeyu. Apo ndeu yafumbi yambani. Anamenyana kwa ma seconds chabe coz anthu analeletsa koma damage inali pamenepo eeeish. Man anali mu dzenje wa mphuno inanyenyeka; wangono yu anavulala pamwendo, bala lowopsa tu. Onse anathamanga nawo ku chipatala, moti coffin amakwilira iwowo kulibe ndithu. Even nkhata pa list anawachotsapo maina awo Zachitika tu dzulo izi
Posted on: Sun, 17 Nov 2013 05:05:02 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015