Ambuye ndi a mayankho:ndinali ndivuto la mmimba vuto limeneli - TopicsExpress



          

Ambuye ndi a mayankho:ndinali ndivuto la mmimba vuto limeneli linayamba ndili standard 2 mchaka cha 1992. makolo anga anakhala akupita nane ku zipatala zosiyana siyana ngakhalenso kwa asinganga koma sizinatheke. ndinafika msinkhu okwatira ndikuvutikabe ndi mmimba.tsiku lina ndinapita kwa msinganga wina.atandiona ananena kuti,bambo munaponyeredwa msempha wa mwana ndipo ndiumene ukukuvutaniwo koma musadandaule ndichosa.anatenda chipaipi chokhala ndi mphanga mkati mwake ndikundiika pa mimba koma chodabwitsa chinali choti sanachisase mkati muja kuti ndi khulupilire kuti munalibe kanthu,atachosa anasasa munagwa zithu zomwe amazinena kuti ndimisemphazo.kunena zoona ine ndinaona kuti zinthuzo zinali misisi yomwe imapezeka pa chinangwa chophika ija.ndikuuzeni ngakhale amanena kuti ndichila sizinali choncho ndakumana ndizambiri koma izi ndikunena kuti anzanga amene mwakumana ndi vuto ndikuma lowera kwa asinganga chonde mubetsa ndalama.nchaka cha 2003 msinganga wina ana ndiuza kuti,pepani achimwene inenso mwana wanga ana mwalira ndi mmimba momwemo ndiye ine ndisakudyereni makobili pitani mukayese kwina, abale anga anada nazo nkhawa koma nanga tikanatani.nchaka 2011 ndi nayamba kupemphera kunyumba kwa abusa ena ake timapemphera mmawa ulionse. 4:30am-5:30am.imene timainena kuti morning devortion.chaka chathachi tinakonza kuti tikhale ndinsonkhano mu july 2014.ndipo anandisankha kuti ndisogolere nsonkhanowo ngati master of ceremonies.ndinasala kudya tsiku limodzi kupempha mulungu kuti azasogolere msonkhanowo komanso kuti andithandize ndisazadwale siku limeneli.litafika siku lija ndina pitirirabe kudwala mmimba mpaka 12:30pm ndipo tinayamba mwambo 1:30pm mpaka 6:00pm koma thawi yonseyi mkuti ine ndilibwino kwambiri.patapita masiku atatu ndinalota tili ku morning devortion kuja tikupemphera kenaka kunazabwera anthu achilendo omwe ananena kuti tikuyenera kulandila mphoto chifukwa cha kupemphelako.choncho anandiuza kuti ndivule malaya nditavula anandiuza kuti ndikweze manja mmwamba,nditakweza manja mmwamba ndinayambakupemphera kwambiri kenaka anthu aja anatenga mipeni ndikundicheka pansi panthiti ndikupitsa mmimba kuchosamo chinthu china chake chokuda atatero anandisoka ndikundiuza kuti basi sindizadwalanso.okondedwa ndikuuzani kuti kuchokera tsiku limeneli sindinadwalenso mmimba mpaka lero.zomwe ndizinthu zomwe sizimatheka.moti ndakhulupilira kuti mulungu sachedwa safulumila.abale ndi alongo ndinaononga ndalama zambili koma osachila koma lero ndachira mwa ulere.TIPEMPHERE:dzikomo atate chifukwa ndinu kasupe wa ma chilitso,ndinu nyanja ya mayankho.ndikupemphera chifukwa cha anthu onse omwe akulimbana ndi mthenda zosiyanasiyana kuti inu muwa tsitsire machilitso,onse omwe ali ndi nkhawa zosiyanasiyana zichokeletu mudzina la yesu khristu.Amen.
Posted on: Sun, 25 Jan 2015 11:10:43 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015