Eti Friday lina lake asilamu ali mu mzikiti akupemphela - TopicsExpress



          

Eti Friday lina lake asilamu ali mu mzikiti akupemphela kunatulukira mdala wina mwa dzidzidzi chikwanje chake chili waliwali. Anangofikila kutsogolo ndi funso Nsilamu ndani muno? Onse kuti ziii. Atafunsanso palibe anayankha. Kenako anangogwila munthu mmodzi mkono ulendo naye mpaka osaonekanso koma palibe anamutsatila. Atafika naye kwao anapeza wamanga mbuzi pa mtengo akuti ndimafuna mundizingile mbuziyi. Atamuzingila anamuuza kuti asendenso. Msilamu uja akuti Iiii inetu kusenda sindimatha koma che Wisiki tawasiya mu mzikiti mommuja. Pamenepo mkulu uja anamusiya wina uja ku nyumba kwakeko ulendonso ku mzikiti konkuja ndi chikwanje chija koma tsopano chili ndi magazi. Asilamu mu mzikiti muja anamuonela patali naganiza kuti wina uja waphedwa ndipo akufuna adzatenge wina. Pomwepo onse anayamba kuimba ma chorus Amayenda ndi Yesu amaone eee! Amaenda ndi yesu amaonekaaaa! Amaoneka mayendedwe.
Posted on: Mon, 04 Nov 2013 19:31:36 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015