GOOD MORNING NDIKUBERENI KA NTHAWI KANU NI MUWERENGE NKHANI - TopicsExpress



          

GOOD MORNING NDIKUBERENI KA NTHAWI KANU NI MUWERENGE NKHANI IYI... Kamwana kena mai ake akhala akudwala nthenda ya mtima kwa kanthawi ndithu. Patha mwezi ali chigonekere kuchipatala koma kamba ka vuto losowa ndalama samathandizidwa ndipo anangotumizidwa kunyumba. Kamwanaka kali kuchipinda kanangomva bambo ake akuwuza anthu kuti mayi ake kuti achire pakufunika chozizwa. Katamva izi kamwanaka kanatenga tindalama tomwe kamasungira kuthamanga wakuma sitolo.Atafika mu sitolo yogulitsira mwankhwala anangotenga tindalama take kuponyera pa kawuntala ndikumuwuza mwini sitolo kuti mundigulitse mankhwala achozizwa. Mwini sitoloyi anadabwitsika ndizochita zamwanayi.Atamufunsa bwino ndi pamene anakhudzidwa ndi nkhani ya mwanayi,pamenepa mwini sitoloyi amanyamuka kupita ku nyumba kwa mwanayi makamakanso powona chikondi chomwe mwanayi anali nacho kwa mayi ake. Mwini sitoloyi anathandiza mayiyu ndi ndalama zochuluka mpaka mayi adapeza bwino. Mwini sitoloyi ndi MULUNGU yemwe amabwera mu njira zosiyanasiyana kutithandiza mavuto athu.Mwanayi ndi unu ndi ine amene tiyenera kudzichepetsa pa maso pa MULUNGU. Matenda a mtima ndi mavuto omwe timakumana nawo mmoyo wathu wa tsiku ndi tsiku ndipo bambo ndi atumiki a MULUNGU omwe akutiuza ife nthawi zonse za njira ya Chauta. Abale ndi alongo Mulungu amadzera mu njira zosayembekezeleka ndikupanga zodabwitsa. Kulionatu tsiku ngati ili ndi chinthu cha mtengo wa patali zedi. Lembani kuti AMEN pomuyamika Mulungu komanso akuchitireni inu zozizwa mmoyo wanu. Admin:AMEN #advisor02
Posted on: Thu, 31 Jul 2014 05:33:45 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015