KUFUNSIRA KWA CHIKHRISTU Atsogoleli: Sister kodi munapeza - TopicsExpress



          

KUFUNSIRA KWA CHIKHRISTU Atsogoleli: Sister kodi munapeza m’bale ngati? Girl: panopa sindikufuna mwamuna. Atsogoleli: Genesesi 2:18 Yehova Mulungu ndipo anati “sikwabwino kuti munthu akhale yekha; ndizampangila omuthangatila iye Girl: Koma nanga poti ine sindimakukondani. Atsogoleli: 1 Yohane 4:8 Iye osakonda sazindikila mulungu;chifukwa mulungu ndiye chikondi. Girl: Koma mukunena zoona atsogoleli? Atsogoleli: Mariko 13:31 Thambo ndi dziko lapansi zidzapita;koma mau anga sadzapita. Girl: IIi koma nthawi yanga siinakwane. Atsogoleli: Mlaliki 3:1 kanthu kalikonse kali ndi nthawi yake ndi chofuna chilichonse cha pansi pathambo chili ndi mphindi yake. Girl: Atsikana onsewa mu churchmu mwasankha ine bwanji? Atsogoleli: Nyimbo ya Solomo 4:7 wakongola monse monse,wokondedwa wanga,namwaliwe, mulibe chilema mwa iwe. Girl: Ine siine okongola. Atsogoleli: Miyambo 31:30 kukongola kungonyenga ,maonekedwe okoma ndi chabe,koma mkazi woopa Yehova adzatamandidwa. Girl: Nde mukufuna nditani? Atsogoleli: 2 Akorinto 2:4 pakuti m’chisautso chambili ndi kuwawa mtima ndinalembela inu ndi misonzi yambili; sikuti ndikumvetseni chisoni, koma kuti mukadziwe chikondi changa kwa inu,chimene ndili nacho koposa. Girl: Hhhhhmmmmm basiiiii... NANENSO NDIMAKUKONDANI
Posted on: Tue, 25 Jun 2013 09:29:38 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015