Ku ntchito kwa Nthabwalist anakonza phwando la mothers day ndipo - TopicsExpress



          

Ku ntchito kwa Nthabwalist anakonza phwando la mothers day ndipo aliyense amayenera kupita ndi banja lake. Nthabwalist, Sitithana mkazi wake komanso Dipuloma ndi Sitithana ana ake anapita monga banja. Atafika Nthabwalist anatenga mikunda iwiri ya Gold label...Sitithana ma botolo awiri a kuchekuche...Dipuloma ndi Sabina anatenga Fanta. Nthabwalist ataledzera anayamba kumunyoza mkazi wake Sitithana pa gulu la anthu amvekere choka mkazi wa ana awiri iwe unatha fasho anthu anaseka koma Sitithana sanayankhe kanthu. Nthabwalist anapitilizabe mkazi wa ana awiri iwe kape ananena izi kambirimbiri komabe Sitithana samayankha kanthu zimangomupwetekera mu mtima. Sitithana anayamba kuledzera ndi Kuchekuche....kenaka Nthabwalist anakuwa ndati unatha fasho iwe mkazi wa ana awiri fotseki! apa Sitithana zinamunyasa kuti Nthabwalist waonjeza naye analankhula mokweza nati chokaaa chimamuna cha mwana mmodzi iweeee anthu onse kuti aaaaaaa Nthabwalist mowa onse mmutu balala anazindikira kuti mwana mmodzi siwake!!
Posted on: Fri, 17 Oct 2014 16:56:11 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015