MNYAMATA WANTHU WA PA CHANCELLOR COLLEGE, AKHOZA KUYIKA DZIKO - TopicsExpress



          

MNYAMATA WANTHU WA PA CHANCELLOR COLLEGE, AKHOZA KUYIKA DZIKO LANTHU LINO LA MALAWI PA MAP, TIYENI TIMUTHANDIZE!! Akulu-akulu, timvetsetsane apa! Si za Chipani izi!! Mwana wanthu-wanthu pa Chancellor College pomwepa wapangidwa shortlisted mu Mpikisano wokhudza za Technology umene Mphoto yake idzakhala yayikulu ndithu ngati atapambana. Mnyamatayu, dzina lake MIXON FALUWEKI ali ndi Project imene wapanga Charger imene waitchula kuti PADOKO Charger. Mu luso limeneli, Charger chakechi chikhoza kuthandiza a Kabaza ku ma Charger ma Phone zimene zikhoza kumawabweletsera ndalama zina zapadela. Akhozanso ku ma Charger ma Torch amene akhoza kumakagwiritsidwa ntchito usiku zimene zikhoza kupangitsa anthuwa kuleka kugula Parrafin. Malingana ndi Proposal Project yakeyi, Mnyamata wanthuyu monga tanena kale wapangidwa shortlist mwa anthu ochepa kwambili 5 muno mu Africa. Chosangalatsa chachikulu, wathuyu ndi yekhayu basi Mmalawi muno kumanso kuchigawo chathu chino cha Africa pakuti enawo ndi Ochokera ku WEST AFRICA. Game ili apa akulu-akulu!! Kuti timuvotele Mnyamatayu. Atawina Mnyamata wanthuyu ndiye kuti Malawi ngati dziko la yiphula. Ndiye tatiyeni tipange zanthu zija za Patriotism zija, tiyeni timuponyele Vote Mnyamatayu popita pa Link ili mmusimuyi. Tikatero, tisinthe from using as Mobile to desktop ngati tikugwiritsa ntchito Phone. Tikavota, chonde tiyeni tipange SHARE pa Time Line yathu kuti azathu awoneko kuti mwina angavote. Tiyeni timukonde mwana wathuyu, tiyeni tilikonde dzikoli. Mnyamata wayinyamula Mbendela ya Fuko uyu! aaas.org/tech-i/vote
Posted on: Tue, 02 Sep 2014 17:33:08 +0000

Trending Topics



:0px; min-height:30px;"> Driving back from KZN last night we experienced very heavy winds

Recently Viewed Topics




© 2015