MSIRIKALI WAMANGIDWA KU ZOMBA Nkhani yomwe yangotipeza kumene - TopicsExpress



          

MSIRIKALI WAMANGIDWA KU ZOMBA Nkhani yomwe yangotipeza kumene ndiyoti msirikali wina ku Zomba ntchito yatha komanso wamangidwa pamene adaphwanya lamulo kuchoka kwa wamkulu wa asirikali. Asirikali wonse dzulo adalamulidwa kuti pasapezeke wina aliyense wokapanga nkhondo ndi apolice kamba ka mkwiyo wa imfa ya mnzawo. Mophwanya lamuloli mmodzi adapitabe ku police la derali kuti akayambe kumenya apolice pa station yonse. Poti adalipo yekha apolice adamuunjilira ndikumugwira ndikupereka lipoti kwa wa mkulu wawo yemwe atafika ku police adangomuuza kuti ntchito yatha ndipo amangidwe kamba koyambitsa chisokonezo komanso kusatsata zomwe adauzidwa dzulo.
Posted on: Fri, 28 Nov 2014 18:27:03 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015