MUNGAMUDZIWE BWANJI MTSOGOLERI WOSATHANDIZA 1. Amakhala chete - TopicsExpress



          

MUNGAMUDZIWE BWANJI MTSOGOLERI WOSATHANDIZA 1. Amakhala chete asilikali ndi apolice akamatibulana mmizindamu. 2. Zinthu zikamalakwika mma ministry monga kuchedwetsa malipiro ama civil servant amangokhala zii osalankhulapo kanthu. 3. Samadziwa malire amudzi wake. Kumufunsa kuti atchule mayina a maboma a dziko lake amakatchulanso chipata. 4. Ma donor amakanirana kumuthandiza. 5. Amakatenga Ndalama za NAC kumapangira function ya mtundu wake kapena kupangira launch organisation ya mkazi wake. 6. Amangolimbana ndi microphone pa podium mmalo moti azingoyankhula. Kumangopanga adjust microphone mpakana kuthyola. 7. Amasokonekera akaona gulu la anthu, mbwelera zimene amakamba zimakhala chifukwa cha mantha ndi gulu. 8. Amayitanitsa atolankhani kuwadyetsa ma sausage, kuwapatsa ma K50,000.00 cholinga atolankhaniwo azilemba zomukomera. 9. Amayamba kudana ndiwachiwiri wake kumakagwirizana ndi mtsogoleri wachipani chake. 10. Amavomereza kuti nkhani zopusa, zopanda mzeru zizingokambidwa pa wayilesi ya boma nthawi iliyonse. 11. Amabera mavoti. 12. Samapita ku maliro amangotumiza nthumwi. 13. Nkhani ikamukulira amakonda kuphafa ndudu za chingambwe osati masewera. 14. Kukonda kumwa madzi pagulu mochititsa manyazi ngati akhuta madziwo mpakana mgwidyo. Kumwa madzi ngati ali ndi drum mmimba.. Ndatchula dzina apa? Ndanyoza munthu ine? Ndatukwana? zinazo wonjezerani.
Posted on: Thu, 27 Nov 2014 18:07:26 +0000

Trending Topics



n-height:30px;">
A seguito dell’imminente Fiera di settembre, ecco le aree che in

Recently Viewed Topics




© 2015