Nkhani yadzulo inandipangitsa kuti ndilankhulane ndi a Henry - TopicsExpress



          

Nkhani yadzulo inandipangitsa kuti ndilankhulane ndi a Henry Chimbali, Mneneri wa unduna wazaumoyo. Nkhani ya Mdulidwe sinkhani yaing‘ono ndipo zoona zake malingana ndi unduna wazaumoyo ndiizi; 1. Mdulidwe Wakuchipatala umachepetsa chiopsyezo chotenga HIV ndi pafupi fupi 60% (thats pafupifupi ndi 60% munthu ukumaziletsa, kuziteteza komnso kupewa njira zina zotengera HIV 2. Ndimdulidwe wakuchipatala chiopsyezo chotenga matenda enawa opatsirana pogonana chimachepanso 3 Mdulidwe wakuchipatala umachepetsa chiopsyezo choti M bambo/ Mnyamata adwale/ ayambe matenda. a Cancer ya chida cha abambo mchingerezi amati Penile Cancer 4. Mnyamata/ m bambo yemwe anapanga mdulidwe wakuchipatala amachepetsa chiopsyezo choti wokondedwa wake adwale/ akhale ndi Cervical Cancer/ Cancer. ya khomo la chiberekero. 5. Mdulidwe umalimbikitsa ukhondo komanso akuti Mnyamata/ M bambo amaoneka bwino zeeedi kapena nditi amaoneka bwino ndithu 5. Nkhani yokwanilitsana ilinso pati? pompo Nde ena mmati bwanji ku Mangochi komwe anthu ambiri anadulitsa kulinso chiwerengero chachikulu cha anthu otenga HIV? Akuti siyense amene anadulitsa amene amachepetsa chiopsyezo. Ngati mdulidwe anapangawo siuli ngati wakuchipatala adakhali pachiopsezobe. Akuti kafuku fuku yemwe anapnga a unduna wa Health akuonetsa kuti chiwerengero cha anthu amene sanadulitse omwe ali/otenga HIV nchokwera kuyerekeza ndi anthu omwe anapanga Mdulidwe ku Mangochiko. Ngati nkotheka PITANI mukadulitse Great Minds kuti muchepetse chiopsyezo chotenga HIV ndi matenda onse ndatchulawo koposa zonse muteteza okondedwa wanu ku Cancer yomwe Ikupha amai ambiiiiiiri Malawi muno. Atsikana tiyeni tilimbikitse okondedwa athu apite kuchipatala akadulitse choooonde. I love you Great Minds and I wish U good health.
Posted on: Wed, 17 Jul 2013 07:38:49 +0000

Trending Topics




© 2015