Nzungu wina ananyamuka ndi galu wake komanso wantchito kukasaka - TopicsExpress



          

Nzungu wina ananyamuka ndi galu wake komanso wantchito kukasaka anyani...cholinga chinali kugwira anyaniwo kuti azikawaweta.. Galuyu anali ophunzitsidwa bwino kagwiridwe kanyani kut asamuvulaze, Atafika kunkhalango nzunguyu anamuuza wantchitoyu kut ndikukwera muntengo ndikakuse anyani, nyani akagwa pansi galuyu azimugwira ku pravate part yake akatero sakhalanso ndi mphamvu ndipo ndizisika kukamugwira nkumuika mu cage iweyo ungokhala ready ndi mfuti basi. Zonse zimayenda bwino kumagwira anyani ndithu, komano wantchitoyu anafunsa... Akut kodi sopano ntchito yanga ndiye ndi chani ndi mfutiyi poti zonse mukuchita nokha? Nzungu anamuuza kut right, iweyo ntchito yako ndiyoti just in case ndagwa muntengomu iweyo uzaombere galu. Nzunguyu anaziwa kale kut ngat sapaganiza bwino tsiku lina atagwa muntengo galu uja akhoza kuzagwira private part yake. Apapa nkhani ndiyoti tiyenera kumakhala anzeru pazina zomwe zingachitike nsogolo... Nzunguyu anagula mfuti kulipira wantchito just in case atagwa muntengo asazapeze vuto. Kodi ife lero just in case titagwa kumwalira tazikonzera kaye oti nkuti pulumutsa..ubale wanzungu ndi galu mumauziwa komabe anaika munthu kut pofuna kupulumuka azamuombere basi, ambiri lero tapanga ubale ndi zinthu zakuziko koma just in case mwa mwalira mukafikira kut. Ahebri 13 vs 14 amanenetsa kut pano tilibe mmudz okhalitsa koma tifunafuna uwo uli nkuzayo.moyo wathu tikukhala mudziko lamavuto limene sizikufunika kukhala popanda oti pulumutsa.tikapanda kuzikonzera lero mmoyo wathu tizasowa chowiringula. Tiyeyeni tifunefune popezeka iye(YESU NKHRISTU) ndikutenga mphamvu zake zikhale ndiife nthawi zonse... Azikudalitsani Adm....#NIBE
Posted on: Thu, 13 Nov 2014 15:20:33 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015