PSI Malawi has launched an SMS based health platform - SUNGA MOYO - TopicsExpress



          

PSI Malawi has launched an SMS based health platform - SUNGA MOYO SERVICE SUNGA MOYO SERVICE (SMS) NDICHANI? Iyi ndi njira yolandilira uthenga wa m’manja wa zaumoyo ya anthu amene afika msinkhu wa ubeleki. Njirayi, imapereka mwayi olandira uthenga wa zaumoyo komanso kuyankha mafunso anu. SMS imagwira ntchito pa nambala za Airtel zokha basi. SUNGA MOYO SERVICE (SMS) - mupezamo uthenga wa: • Njira za kulera zosiyanasiyana • Ubwino ogwiritsa ntchito njira zakulera • Ndondomeko ya kagwiritsidwe ntchito ka njira zosiyanasiyana zakulera • Mauthenga a tsopano a za kulera 1. Kagwiritsidwe ntchito ka SMS - Tumizani MOYO ku 50051 - Sankhani chilankhulo chomwe mukufuna - Pitilizani monga mwa ndondomeko yotsatirayi 2. Gawo lililonse, lidzikupatsani mwawi obwerela ku tsamba loyamba, potumiza 00. NCHIFUKWA CHANI NDIKUYENERA KUGWIRITSA NTCHITO SMS? • Chifukwa chakuti mumasamalira banja lanu, ndikuti likhale la umoyo wabwino • Chifukwa uthenga wake ndiwodalilika, wachindunji komanso woyenelera • Chifukwa Sunga Moyo ndiwaulele • Chifukwa Sunga Moyo ndiwosavuta kugwiritsa ntchito • Chifukwa SMS munkhonza kugwiritsa ntchito pa foni iliyonse yam’manja. Ngati mufuna kudziwa zambiri, tumizani sms ya funso lanu ku 50051 ndipo mudzayankhidwa.
Posted on: Thu, 08 Aug 2013 13:33:03 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015