Pamene ndidali mphunzitsi Ndidatenga transfer kupita ku China - TopicsExpress



          

Pamene ndidali mphunzitsi Ndidatenga transfer kupita ku China kukapitiriza kuphunzitsa cause ndidamva kuti aphunzinsi amalipidwa bwino kumeneko. Tsiku loyamba kulowa mclass, ndidayamba ndi kuitana register. Ndidati, Sheng! Ophunzira adayankha, Present! Ndidaitana dzina lachiwiri, Chu Muon. Ophunzira wina adayankhanso, Present! Kenako,ndidayatsamula, Hatchia!,Ophunzira wina amene adakhala pakona adayankha, Present! Ndidadzuma, Hmmmm... Ophunzira onse adakuwa, Absent! Ndidazunguzika mutu nawayangana onse ndi chidwi, Shaa... Ophunzira atatu anayima nafunsa,ndani mwa ife? Ndidazunguzika mutu kwambiri nafunsa, What is wrong? Ophunzira wina anaimilira, Sir, Im not Wrong, Im called Wong. Ndidaseka, Hahahaha! Nsikana wina adayankha, Present sir! Ndidayandikira pafupi kuti ndionetsetse kuti chikuchitika ndi chani. Pamene ndimasuntha,pen yanga idagwa kuchokela pa desk nkupanga sound, Ping chung chong! Mnyamata wina adaima nayankha, Present sir! Ndidazunguzika mutu kwambiri, ndidakhumudwa, nkuthawiranso ku Malawi!
Posted on: Tue, 06 Jan 2015 12:17:01 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015