Pemphero la sena pa kudya: ndikuthokozan mbuyanga pazonse zomwe - TopicsExpress



          

Pemphero la sena pa kudya: ndikuthokozan mbuyanga pazonse zomwe mudatchitira, mwatipasa nsima imeney ya mnsiku larero. Ndiwo yake sindiwo wamba ayi, tiku2okozan mbuye potipasa ndiwo ya nkhuku. Nkhuku iyi mudayiyang,anira iyi ili mwana, mphamba kubwera kut ayikwatule koma inu mudaiteteza ,tikapisaso mbale tikuona kut tomato alimo tikuyamikani mbuya2 powateteza azimay omwe adakatenga matimatiwa kuchikanga, galimoto atrafc akadaiphata koma inu mudaiteteza, tikaonesesa bwinobwinombo atenga moyo alipo, mafuta akaznga alowamo, tikupemphererambo kampan iyi ya uniliva yomwe imbapanga kazinga, kut ipitilize. kufiraku tikuonanso kut loyco walowamo mwadalitse madalitso akupitirira kut awonjezere pomwe achotsa. Pomaliza tikupempha zonsez muzina lamwana wanu uyu, uyu, mban? Uyu mwana wanu wakubadwa yekha, mban uyu, uyu mwana adakhomera pa mtanda, uyu mwana adapita kuukwat adasandutsa madzi kukhala vinyu uyu, tso uyu adapempherera akhungu adamuuza penya iye adawona. Kamwana kamvekere yosefe? Ayi amenewo ndi babache tikufuna mwana. Uyu mban uyu #chindinho
Posted on: Thu, 31 Oct 2013 19:36:40 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015