Tengerani chitsanzo cha masapota a Bullets,Butao auza masapota a - TopicsExpress



          

Tengerani chitsanzo cha masapota a Bullets,Butao auza masapota a wanderers. #Namzy. Mlembi wa timu ya Mighty wanderers a Mike Butao wapempha masapota a timuyi kuti azitengapo gawo lalikulu potandiza timuyi pa nkhani ya ndalama.Chifukwa china chimodzi timu yathu isakuchita bwino ndikusatengapo gawo kwa masapota athu poyipangira timu ndalama. Ndikupempha osatira a Wanderers kuti atengere chitsanzo cha masapota a Bullets pothandiza timu yawo ngati mmene amachitira mu sapota mapeto,anatero Butao. Butao watinso zomwe akuchita masapota a Bullets pomatengapo gawo pothandiza timu yawo zapangisa timuyi kuchita bwino kwambiri season ino. Bullets ikuchita bwino lero chifukwa cha masapota ake nkona inagura osewera a pamwamba ndipo ikukolora zomwe inafesa nde ndikupempha masapota athu atengere zimenezo,anatero Butao.
Posted on: Fri, 07 Nov 2014 07:43:56 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015