.........MULUNGU ALI NNJIRA ZAKE...... panali dziko lina - TopicsExpress



          

.........MULUNGU ALI NNJIRA ZAKE...... panali dziko lina lake,mdzikoli linali ndi mtsogoleri ovuta zedi moti munthu akalakwa amakathera komweko...Nde munali munthu wina amene anali ndi mphatso yapadera,iyeyu amatha kulemba signature ya munthu aliense ingakhale ya mtsogoleri wa dziko lake..mukudziwa munthu sakhala wa bwino kose anthu ena sanali kumufunira zabwino mkuluyi chifukwa cha mphatso yache, Nde anagwirizana kuti akamunenere kwa mtsogoleri wawo amene ali wa mkhanza ndipo anatero. Mtsogoleri anatuma asirikari ake nakamumanga munthuyi,anafika anafunsidwa mafuso motere: Mtsogoleri:kodi ndiwe amene ukumamasaina signature yanga? Oimbidwa:eya ndine amene ndipo ya wina aliese ndimaitha Mtsogoleri:tasaina apa ndione Oimbidwa:kusaina Mtsogoleri:aaaah!eti wakwanisadi,iwe basi ukhala otsatira wanga amene uzisaina mapepala onse ofunikira kusaina ine chifukwa nthawi zambiri ndimakhala otanganidwa.. Anthu amulungu inde ndiziwa ndipo ndimakhulupirira aliense anamunikha luso lake lake mwapadera koma sionse amene amakufunirani/kukusangalalirani za luso lomwe muli nayo mokuti ali kalikiliki kuesaesa kufuna atakupherani za mtsogolo yanu,, Koma musakadere nkhawa za iwo coz amene ali ndi inu simuthu ndipo ngati iri mphatso yochokera kwa iye palibe azakuchotsereni ndipo PAMENE AKUKUFUNIRANI ZOIPA NDI PAMENE MPHATSO YANU IZAKHALE IKUPITIRIRABE koma ngati ziri zochoka kwa munthu ZIZAKUKANIKANI TSIKU LINA.. Kakondwereni ndikugwirisa bwino ntchito luso anakupasani. MULUNGU odziwa kulalikira akapitireze kulalikira mkati mwa mitima yanu,,Amen.. Tsiku labwino kwa nonse mwa ambuye..
Posted on: Thu, 08 Jan 2015 05:13:29 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015