Ndine mwamuna wa zaka 26 ndipo ndimakhala kuno ku Chileka, mboma - TopicsExpress



          

Ndine mwamuna wa zaka 26 ndipo ndimakhala kuno ku Chileka, mboma la BT. Ndili single koma ngakhale ndimagwira ntchito. Ndili ndi mzanga amene anakwatira. Mzanga yu akazi ake amangokhalira kuwazunza. Kuwamenya ndiye samati wawamenya liti. Koma tu ndi mkazi wowoneka bwino kaya mzanga yu amapangiranji izi kaya. Tsopano vuto ndiloti mkazi yu amabwera kuzandidandaulira ineyo zimene amakumana nazo. Ndiye pano ndayamba kumamufila. Mpakana pena maganizo akumandibwelera oti ndingothawa naye ndimukatire koma ndizikakhala kwina. Maganizo ena akumandiuza kuti ndikuyenera kulemekeza friendship imene ili pakati pa awirife. Kodi pamene nditani? Geoffrey Chitosi Chileka Blantyre (Kwawo kwa Ma Blacks)
Posted on: Tue, 05 Nov 2013 16:21:20 +0000

Trending Topics



Recently Viewed Topics




© 2015